TSIKU LOKUMBUKIRA NTCHITO YOLIMBANA NDI ZIPHUPHU

M’chaka cha 2003, msonkhano wa maiko a United Nations unakhazikitsa 9 December
kukhala tsiku lokumbukira ntchito yolimbana ndi ziphuphu ndi katangale pa dziko lonse.
Ku Malawi kuno, tsikuli chaka chino tilikumbukira pa mutu wakuti “UMUNTHU;
GWERO LA MALAWI WOPANDA ZIPHUPHU.”

Mwambo waukulu chaka chino okumbukira tsikuli udzachitika pa 9 December, 2021, ku
Grand Palace Hotel ku Mzuzu kuyambila nthawi ya 9 koloko m’mawa mpaka 12:30
masana.
Cholinga chokumbukira tsikuli ndikufuna kuzindikiritsa anthu onse zakuipa kwa
mchitidwe wa ziphuphu ndikuwalimbikitsa kuti atengepo mbali pothetsa ziphuphu.
Lisanafike tsikuli, kwakhala zochitika m’mwezi odziwitsa anthu za kuipa kwa ziphuphu
ndi Katangale zomwe zakhala zikuchitika m’maboma osiyanasiyana m’dziko muno
kuyambira pa 8 Novembala mpaka pa 8 Disembala, 2021. Kudzakhalanso ulendo wa
ndawala mumzinda wa Mzuzu.

Pa 9 Disembala kudzakhala mwambo waukulu okumbikira tsikuli ndi msonkhano
wokambirana nkhani zolimbana ndi ziphuphu. Nonse mukulimbikitsidwa kutenga nawo
mbali pa zochitikazi kudzera pa wailesi ndi kanema wa MBC. Tiyeni tikhale ndi umunthu,
tithane ndi ziphuphu ndi kupanga Malawi wabwino.

 

 

MARTHA CHIZUMA
DIRECTOR GENERAL

Scroll to Top