TSIKU LOKUMBUKIRA NTCHITO YOLIMBANA NDI ZIPHUPHU PA DZIKO LONSE

M’chaka cha 2003, msonkhano wa maiko a United Nations unakhazikitsa 9 December kukhala tsiku lokumbukira ntchito yolimbana ndi ziphuphu ndi katangale pa dziko lonse.

Ku Malawi kuno tsikuli chaka chino likumbukiridwa pa mutu wakuti “TICHITEPO KANTHU; TITHANE NDI ZIPHUPHU TIMANGE MALAWI WABWINO.”

 Bungwe la Anti-Corruption Bureau likudziwitsa anthu onse kuti mwambo wa chaka chino okumbukira tsikuli udzachitika pa 9 December, 2020, ku Mount Soche Hotel m’boma la Blantyre kuyambila nthawi ya 9 m’mawa mpakana 12:30 masana.

 Cholinga chokumbukira tsikuli ndikufuna kuzindikiritsa a Malawi onse zakuipa kwa mchitidwe wa ziphuphu ndikuwalimbikitsa kuti atengepo mbali pothetsa ziphuphu.

Lisanafike tsikuli kunali zochitika mmwezi odziwitsa anthu zakuipa kwa ziphuphu ndi Katangale zomwe zinachitika m’maboma osiyanasiyana m’dziko muno kuyambira pa 9 Novembala mpaka pa 8 Disembala.

Pa 9 December kudzakhala kukumbikira tsikuli ndi msonkhano wokambilana nkhani zolimbana ndi ziphuphu. Nonse mukuitanidwa. Tiyeni tigwirizane kuti kuthane ndi ziphuphu ndi kumanga Malawi wabwino.

REYNECK MATEMBA

DIRECTOR GENERAL

Scroll to Top