Bungwe la United Nations lidakhazikitsa tsiku la padera lokumbukira ntchito yothana ndi ziphuphu ndi katangale pa dziko lonse la pansi (International Anti-Corruption Day) pambuyo pakuti maiko ndi zilumba zokwana 190, kuphatikizapo Malawi, zitavomereza pa mkumano umene anali nawo mchaka cha 2003 otchedwa United Nations Against Corruption (UNCAC), mchingerezi. Bungweli linakhazikitsa 9 December kukhala tsiku la paderali. Cholinga chake ndi kulimbikitsa anthu onse kudziwa kuopsa kwa mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale komanso kulimbikitsa aliyense kutenga nawo gawo polimbana ndi mchitidwewu.
Motsogozedwa ndi Bungwe la United Nations on Drugs and Crime (UNODC), tsikuli lidzakumbukiliridwa ndi mutu wakuti: “Kugwirana Manja ndi Achinyamata Polimbana ndi Ziphuphu ndi Katangale: Kupanga Tsogolo la Umphumphu.” Kampeniyi ikuvomereza gawo lalikulu limene achinyamata ali nalo pa kulimbikitsa umphumphu, kufalitsa uthenga wa kuopsa kwa ziphuphu ndi katangale komanso kupereka njira za makono zoletsera mchitidwewu. Popeza padziko lapansi pali achinyamata pafupifupi 1.9 biliyoni, bungwe la United Nations likupempha kuti achinyamata alimbikitsidwe ndi kupatsidwa mphamvu kuti akhale oteteza choonadi, chilungamo, ndi udindo m’madera awo.
Ku Malawi, tsikuli likukumbukiridwa pansi pa mutu wakuti: “Kulimbikitsa kulemekezana pa Nkhondo Yolimbana ndi ziphuphu ndi katangale,” womwe watengedwa ku mutu wa African Union wa chaka cha 2025. Mitu yonse iwiri, wa United Nations ndi African Union, ikutithandiza kudziwa kuti kuthana ndi ziphuphu ndi katangele, kuposerapo pa kuteteza chuma cha dziko, kukuphatikizanso kuteteza umphumphu, ulemu komanso ufulu wa munthu wina aliyense. Pamodzi, mituyi ikulimbikitsa kuchitapo kanthu makamaka kwa achinyamata, kuti amange dziko lachilungamo, losakondera anthu, komanso lopanda ziphuphu and katangale.
Pokonzekera mwambo waukulu umene udzachitike lachiwiri pa 9 December 2025 ku Bingu International Convention Centre (BICC) mzinda wa Lilongwe, bungwe la Anti-Corruption Bureau (ACB) lakhala likupangitsa zochitika zosiyansiyana ndi mabugwe amene sali a boma, ma department aboma (pogwiritsa ntchito ma komiti opititsa patsogolo ungwiro mu nthambi zosiyanasiyana za boma), anzathu owona zomenyera ufulu wa anthu, achinyamata, ndi anthu osiyanasiyana monga mbali imodzi yolimbikitsa mgwirizano pothana ndi mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale komanso kuonetsetsa kuti umphumphu wakhazikika pakati pathu.
Pa 9 December 2025 padzakhala zochitika monga izi:
a) Kukambirirana pakati pa akatswiri opereka ntchito kwa anthu omwe adzafotokoze mavuto amene anthu amakumana nawo akamafuna kuthandizidwa
b) Kuonetsa ntchito zimene makomiti aboma opititsa patsagolo ungwiro amapereka kwa anthu ndi cholinga chofuna kuthandiza kudziwitsa poyera udindo wa opereka ntchito ndi othandizidwa.
c) Kuthokoza ena mwa ma komiti opititsa patsogolo ungwiro mumadipatimenti aboma pa ntchito yomwe agwira mchakachi.
d) Tidzalandira mauthenga ochokera kwa atsogoleri osiyanasiyana, magule olimbikitsa zachikhalidwe komanso oyimba kwaya yolimbikitsa chikhalidwe chaumphumphu.
Kudzera mu mwambowu, Boma la Malawi lidzakhala likukumbutsa anthu onse, makamaka achinyamata, kuti ndi udindo wa tonse ndiponso ndi tsinde ya nsanamila ya chikhalidwe chabwino kuthana ndi ziphuphu ndi katangale. Dziwani kuti kutenga mbali kwanu ngati munthu ngakhale mutachita zochepa kudzathandiza Malawi monga dziko, kuchirikiza chikhalidwe chaumphumphu ndi chapamwamba mosakondera. Aliyense akhale ndi udindo owonetsetsa kuti umphumphu ndi chikhalidwe changwiro zikupita patsogolo.
Bungwe la Anti-Corruption Bureau likutilimbikitsa tonse kutenga nawo mbali yolimbikitsa ulemu pa Nkhondo Yolimbana ndi Ziphuphu ndi Katakhale kuti tikhale ndi Malawi opambana, olimbikitsa chilungamo komanso umphumphu.
GABRIEL CHEMBEZI
ACTING DIRECTOR GENERAL
